Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini.
1 Samueli 10:20 - Buku Lopatulika Chomwecho Samuele anayandikizitsa mafuko onse a Israele, ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Samuele anayandikizitsa mafuko onse a Israele, ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Samuele adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele, ndipo pochita maere, fuko la Benjamini ndilo lidasankhidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa. |
Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini.
Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.
Za Benjamini anati, Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika; am'phimba tsiku lonse, inde akhalitsa pakati pa mapewa ake.
koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.
Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; ndipo anayandikizitsa banja la Amatiri, mmodzimmodzi; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.
Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli choipa ichi lero.
Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka.