1 Samueli 14:41 - Buku Lopatulika41 Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa41 Nchifukwa chake Saulo adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani simudandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati wolakwa ndineyo kapena mwana wanga Yonatani, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, aoneke ndi Urimu. Koma tchimolo likakhala la Aisraele, aoneke ndi Tumimu.” Maere adagwera Yonatani ndi Saulo, anthu nkupulumuka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Ndipo Sauli anapemphera kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, “Chifukwa chiyani simunandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati tchimoli lipezeka ndi ine kapena ndi Yonatani mwana wanga, Inu Mulungu wa Israeli, aoneke ndi Urimu. Koma ngati wochimwa ndi anthu anu, Aisraeli aoneke Tamimu.” Maere anagwera Sauli ndi Yonatani ndipo anthu anapezeka osalakwa. Onani mutuwo |