Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli choipa ichi lero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli choipa ichi lero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Apo Saulo adati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu. Tiwone ndi tchimo lanji lachitika lero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Choncho Sauli anati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu, ndipo tiyeni tione kuti kodi tchimo limeneli lachitika bwanji lero?

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:38
11 Mawu Ofanana  

Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mzinda.


Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo.


Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;


Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao.


Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.


Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa