Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:39 - Buku Lopatulika

39 Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Pali Chauta, Mpulumutsi wa Aisraele, wochimwayo ngakhale akhale mwana wanga Yonatani, afe ndithu.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo amene adamuyankha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Pali Yehova amene amapulumutsa Israeli, ngakhale tchimolo litapezeka ndi mwana wanga Yonatani, iye afe ndithu.” Koma palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthuwo amene anamuyankha.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:39
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha;


Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.


Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira.


Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya.


Ndipo iye ananena ndi Aisraele onse, Inu mukhale mbali ina, ndipo ine ndi Yonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, Chitani chimene chikukomerani.


Pamenepo Saulo anati, Mulungu andilange, naonjezereko, pakuti udzafa ndithu, Yonatani.


Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye.


Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.


Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako.


Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa