Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo Saulo anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israele kodi? Koma Iye sanamyankhe tsiku lomweli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo Saulo anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israele kodi? Koma Iye sanamyankhe tsiku lomweli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Tsono Saulo adafunsa Mulungu kuti, “Kodi tiŵalondole Afilistiŵa? Kodi muŵapereka m'manja mwathu?” Koma Mulungu sadamuyankhe kanthu tsiku limenelo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Choncho Sauli anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndiwatsatire Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwathu?” Koma Mulungu sanamuyankhe tsiku limenelo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:37
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.


Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, Iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawatulukire pandunji pa mkandankhuku.


Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israele, Funsira ku mau a Yehova lero.


Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova.


Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?


Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.


namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.


Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.


Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila.


Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.


Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa