Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 10:21 - Buku Lopatulika

21 Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; ndipo anayandikizitsa banja la Amatiri, mmodzimmodzi; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Adasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja, ndipo pochita maere, banja la Matiri ndilo lidasankhidwa. Potsiriza pake adasonkhanitsa anthu a m'banja la Matiri mmodzimmodzi, ndipo pochita maere, Saulo mwana wa Kisi, ndiye adasankhidwa. Koma pamene adamfunafuna, sadampeze.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 10:21
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini.


Maere aletsa makangano, nulekanitsa amphamvu.


Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.


Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai.


Chomwecho Samuele anayandikizitsa mafuko onse a Israele, ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa.


Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.


Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu ena onse anamlekeza m'chifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa