Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yona 1:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Amalinyerowo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tichite maere kuti tipeze amene wabweretsa masoka ameneŵa.” Choncho adachitadi maerewo, ndipo adagwera Yona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo oyendetsa sitimayo anayamba kuwuzana kuti, “Bwerani, tichite maere kuti tipeze amene wabweretsa tsoka limeneli.” Iwo anachita maerewo ndipo anagwera Yona.

Onani mutuwo Koperani




Yona 1:7
18 Mawu Ofanana  

Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, chaka chakhumi ndi chiwiri cha mfumu Ahasuwero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara.


Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse; mundidziwitse chifukwa cha kutsutsana nane.


Agawana zovala zanga, nachita maere pa malaya anga.


Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse.


Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.


Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere:


Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri mu Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa