Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 1:24 - Buku Lopatulika

Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atamuletsa kuyamwa, adapita naye ku nyumba ya Chauta ku Silo. Adatenga ng'ombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogramu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Ngakhale mwanayo anali wamng'ono ndithu, adapita nayebe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo.

Onani mutuwo



1 Samueli 1:24
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.


Ndipo mbale wa Tapenesi anamuonera Genubati mwana wake, ameneyo Tapenesi anamletsera kuyamwa m'nyumba ya Farao, ndipo Genubati anakhala m'banja la Farao pamodzi ndi ana aamuna a Farao.


Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.