Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mwanayo adakula, ndipo pa tsiku lakuti amuletsa kuyamwa, Abrahamu adachita phwando lalikulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:8
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.


Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna mu ukalamba wake.


Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.


Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.


Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.


Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake.


Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero.


Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.


chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake,


Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.


Ataleka tsono kuyamwitsa Wosachitidwa-chifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna.


Ndipo atate wake anatsikira kwa mkazi; ndi Samisoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata.


Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu;


Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.


Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.


Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa