1 Samueli 1:12 - Buku Lopatulika Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyo akupemphera chotero pamaso pa Chauta, Eli ankamuyang'ana pakamwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akupemphera choncho kwa Yehova, Eli ankamuyangʼana pakamwa. |
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.
nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.
Koma Hana ananena mu mtima; milomo yake inatukula, koma mau ake sanamveke; chifukwa chake Eli anamuyesa woledzera.