ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe.
1 Akorinto 7:4 - Buku Lopatulika Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso. |
ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe.
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.