Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.
1 Akorinto 11:2 - Buku Lopatulika Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikukuyamikani chifukwa mumandikumbukira pa zonse, ndipo mumasunga miyambo imene ndidakusiyirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani. |
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.
Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.
umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.
Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo mu Mipingo yonse.
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse.
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu;
Chifukwa chake tsono, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata yathu.
Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.