Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 11:17 - Buku Lopatulika

17 Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Tsopano pali mfundo ina imene sindingakuyamikireni. Ndiye kuti misonkhano yanu imabweretsa zoipa osati zabwino ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 11:17
14 Mawu Ofanana  

Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.


Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.


Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo:


Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu.


Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;


Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.


Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.


Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?


Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.


osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.


kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa