1 Akorinto 11:22 - Buku Lopatulika22 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Zokuwonerani zimenezi! Kodi mulibe nyumba zomakadyeramo ndi kumweramo? Kodi kapena mufuna kunyazitsa Mpingo wa Mulungu ndi kuŵachititsa manyazi amene alibe kanthu, eti? Ndikuuzeni chiyani tsono? Ndingakuyamikeni ngati? Iyai, pa zimenezi sindingakuyamikeni konse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni. Onani mutuwo |