Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 93 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 93

Ufumu wa Mulungu ndiwo wa ulemerero, mphamvu, ndi chiyero

1 Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.

2 Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija; Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe.

3 Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wao; mitsinje ikweza mafunde ao.

4 Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja.

5 Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi