Alemekeza Mulungu pa ntchito zao zazikulu zokoma1 Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano. 2 Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo. 3 Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu: Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha. 4 Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma. 5 Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha. 6 Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake, pakuwapatsa cholowa cha amitundu. 7 Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo; malangizo ake onse ndiwo okhulupirika. 8 Achirikizika kunthawi za nthawi, achitika m'choonadi ndi chilunjiko. 9 Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa. 10 Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi