Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 9:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira padziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsiku limenelo Chauta, Mulungu wao, adzaŵapulumutsa, pakuti anthu akewo ali ngati nkhosa. M'dziko laolo anthuwo adzakhala onyezimira ngati miyala ya mtengo wapatali ya pa chisoti chaufumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa pakuti anthu ake ali ngati nkhosa. Adzanyezimira mʼdziko lake ngati miyala yokongola pa chipewa chaufumu.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 9:16
25 Mawu Ofanana  

Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.


Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.


Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulochepo maina a ana a Israele;


Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye.


Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.


Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wachifumu m'dzanja la Mulungu wako.


Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipirikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso kumakola ao; ndipo zidzabalana ndi kuchuluka.


Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutali; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israele adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa achita ndi zoweta zake.


Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m'dzanja la iye amene anamposa mphamvu.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.


Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.


Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.


Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.


Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.


Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.


Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.


Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.


Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.


Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa