Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 8:6 - Buku Lopatulika

6 Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Ngakhale ziwoneke ngati zosatheka kwa anthu a m'fuko limeneli amene adzatsale nthaŵi imeneyo, kodi zimenezi zidzakhalanso zosatheka ndi kwa Ine ndemwe?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati zikuoneka kuti nʼzosatheka kwa anthu otsala pa nthawi ino, kodi zidzakhala zosathekanso kwa Ine?” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 8:6
13 Mawu Ofanana  

Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.


Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.


Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu.


Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;


Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondikanika Ine?


Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirire mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake.


Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.


Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa