Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikapo nyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 4:2
19 Mawu Ofanana  

mwa kulemera kwakenso cha zoikaponyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikaponyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikaponyali chilichonse;


nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.


Ndipo anapanga zoikaponyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika mu Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.


chingwe chasiliva chisanaduke, ngakhale mbale yagolide isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanathyoke kuchitsime;


Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.


Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikaponyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso:


Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wake mikono makumi awiri, ndi chitando chake mikono khumi.


Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa