Zekariya 14:2 - Buku Lopatulika2 Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mzindawo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mzinda lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mzindamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa. Onani mutuwo |