Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 1:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 “Pambuyo pake m'masomphenyanso ndidaona nyanga zinai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kenaka ndinayangʼananso, ndipo patsogolo panga panali nyanga zinayi.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 1:18
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.


Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.


Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m'dzanja lake.


Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka.


Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anatuluka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nchiyani ichi chilikutulukachi.


Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati padziko ndi thambo.


Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa.


Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa