Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Zekariya 1:17 - Buku Lopatulika

17 Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Ulengezenso kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “M'mizinda yangayi mudzakhalanso chuma chambiri. Ndidzasangalatsanso Ziyoni, ndipo Yerusalemu ndidzamsandutsanso mzinda wanga wapamtima.” ’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 1:17
33 Mawu Ofanana  

Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.


Ndi Aisraele otsala ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'cholowa chake.


Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni.


Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga mizinda ya Yuda; ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao.


Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.


Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;


Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.


Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.


M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.


Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima mu Yerusalemu.


Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.


M'mizinda ya kumtunda, m'mizinda ya kuchidikha, m'mizinda ya kumwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'mizinda ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova.


Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.


Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukuchotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'mizindamo; ndi pamabwinja padzamangidwa.


Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mizinda ya mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.


Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala mu Sefaradi adzakhala nayo mizinda ya kumwera, cholowa chao.


Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, fuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikulu.


Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.


Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu.


nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa