Zefaniya 3:11 - Buku Lopatulika11 Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 “Tsiku limenelo inu a ku Yerusalemu simudzachitanso manyazi, chifukwa cha zoipa zonse zimene mudandichita, zimene mudandipandukira nazo. Pakuti nthaŵi imeneyo ndidzakuchotserani onse odzikuza ndi onyada. Simudzachitanso zonyada zanuzo pa phiri langa loyera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Tsiku limenelo simudzachita manyazi chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira, popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo. Simudzakhalanso odzikuza mʼphiri langa lopatulika. Onani mutuwo |