Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 2:11 - Buku Lopatulika

11 Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya pa dziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Motero Chauta adzaŵaopsa kwambiri. Adzaononga milungu yonse ya pa dziko lapansi. Mitundu yonse ya anthu idzampembedza Chauta, mtundu uliwonse ku dziko lakwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yehova adzawachititsa mantha kwambiri pamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo. Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira, uliwonse ku dziko la kwawo.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 2:11
36 Mawu Ofanana  

Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.


Mafumu onse a padziko lapansi adzakuyamikani, Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.


Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.


Ndimo mafano adzapita psiti.


Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.


Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.


Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;


Muzitero nao, milungu imene sinalenge miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati, Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;


Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake.


Pakuti ndidzachotsa maina a Abaala m'kamwa mwake; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao.


ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?


Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala mu Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;


Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Atero Yehova wa makamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m'mizinda yambiri adzafika,


Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.


Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera, nimwa vinyo wa nsembe yao yothira? Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa