Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 2:10 - Buku Lopatulika

10 Ichi adzakhala nacho m'malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ichi adzakhala nacho m'malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chimenechi chidzakhala chilango choyenerera kunyada kwaoko, chifukwa adanyoza anthu a Chauta Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo, chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 2:10
18 Mawu Ofanana  

Sanalole munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa;


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?


Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.


Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.


Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo?


Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.


Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukire chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kuvina, ndi kukondwera ndi chipeputso chonse cha moyo wako, kupeputsa dziko la Israele,


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m'zipata zake achilendo, nachitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.


Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?


Ndinamva kutonza kwa Mowabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa