Zefaniya 2:9 - Buku Lopatulika9 Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikulumbira kuti, Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo wa Israele, Amowabu adzaonongedwa ngati anthu a ku Sodomu, Aamoni adzaonongedwa ngati anthu a ku Gomora. Malowo adzakhala ngati dera la zitsamba za khwisa ndi la nkhuti za mchere, dziko lachipululu mpaka muyaya. Otsala mwa anthu anga adzafunkha malowo. Opulumuka a mtundu wanga adzalandira malowo ngati dziko lao.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Choncho, pali Ine Wamoyo,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, “Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu, Amoni adzasanduka ngati Gomora; malo a zomeramera ndi maenje a mchere, dziko la bwinja mpaka muyaya. Anthu anga otsala adzawafunkha; opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.” Onani mutuwo |