Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 1:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala mu Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Ndidzasamula dzanja langa kuti ndilange anthu a m'dera la Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu. Ndidzafafaniziratu zotsalira zonse za Baala pa malo ano. Palibe aliyense amene adzakumbukirenso ansembe a fanolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala, mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 1:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.


Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.


Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.


Mwatambasula dzanja lanu lamanja, nthaka inawameza.


Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.


Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.


chifukwa chake taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale chofunkha cha amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.


ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako.


Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.


Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa