Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 1:3 - Buku Lopatulika

3 Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Ndidzafafaniziratu anthu ndi nyama zomwe. Ndidzaononga mbalame zamumlengalenga ndi nsomba zam'nyanja. Ndidzagwetsa anthu ochimwa. Ndidzafafaniziratu mtundu wa anthu kuti usaonekenso pa dziko lapansi,” akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe; ndidzawononga mbalame zamlengalenga ndi nsomba za mʼnyanja. Ndidzawononga anthu oyipa, ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 1:3
22 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.


Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.


Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka mizinda ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,


ndipo Yehova wasunthira anthu kutali, ndi mabwinja adzachuluka pakati padziko.


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.


Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala chokhumudwitsa cha mphulupulu cha nyumba ya Israele, chifukwa chake ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.


Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao.


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


Efuremu adzati, Ndili ndi chiyaninso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndili ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zochokera kwa Ine.


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.


Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,


Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.


Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa