Yoweli 3:2 - Buku Lopatulika2 ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse, ndipo ndidzaŵatengera ku chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzaŵaweruza chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, osankhidwa anga, pakuti adaŵamwaza m'maiko ao onse, nagaŵana dziko langa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzawaweruza chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli, pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu ndikugawa dziko langa. Onani mutuwo |