Yoweli 2:23 - Buku Lopatulika23 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere mu Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 “Inu anthu a ku Ziyoni, kondwani ndi kusangalala chifukwa cha zimene Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani. Wakukomerani mtima pokupatsani mvula mofulumira. Wakupatsani mvula yochuluka, kumayambiriro ndi kumathero, monga pa masiku amekedzana. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani, kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu, pakuti wakupatsani mvula yoyambirira mwachilungamo chake. Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka, mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja. Onani mutuwo |