Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 2:22 - Buku Lopatulika

22 Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Inu nyama zakuthengo, musaope, pakuti msipu wakuchipululu akuphukira. Mitengo ikubala zipatso. Mkuyu ndi mpesa zikubereka kwamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Inu nyama zakuthengo, musachite mantha, pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira. Mitengo ikubala zipatso zake; mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 2:22
25 Mawu Ofanana  

pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi.


Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.


Akukha pa mabusa a m'chipululu; ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe.


Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira.


Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.


Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.


Ndipo ndidzachulukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso chitonzo cha njala mwa amitundu.


Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edeni ndi mizinda yamabwinja, ndi yachipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo.


Koma inu, mapiri a Israele, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israele zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.


ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?


pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku choponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha.


Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.


Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa