Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 1:18 - Buku Lopatulika

18 Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Zoŵeta zikulira ndi njala. Ng'ombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa choti zilibe busa. Nazonso nkhosa zikusauka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Taonani mmene zikulirira ziweto; ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa zilibe msipu; ngakhalenso nkhosa zikusauka.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 1:18
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.


Ndipo mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye linali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'chipululu.


Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.


Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao;


M'mwemo chifukwa cha inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zake.


Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa