Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 3:3 - Buku Lopatulika

3 nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 namauza anthu kuti, “Mukadzaona ansembe Achilevi aja atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, mudzanyamuke pamalo panu ndi kuŵatsata.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 kulangiza anthu kuti, “Mukaona ansembe a Chilevi atanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu, inu munyamuke pa malo ano ndi kumalitsatira.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 3:3
20 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi chonenepa china.


Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.


Ndipo akulu onse a Israele anadza, ansembe nanyamula likasa.


ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse.


Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako.


Mose anauza Alevi akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kuti,


Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele.


Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapite njirayi kufikira lero.


Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu.


Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima mu Yordani.


Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.


Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.


Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolide, naziika pamwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa