Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 2:4 - Buku Lopatulika

4 Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwe uko afuma;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma pamenepo mkaziyo nkuti ataŵatenga amuna aŵiriwo naŵabisa, motero adayankha kuti, “Zoonadi kunyumba kwanga kuno kudaabwera anthu ena, koma kumene ankachokera, sindikudziŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Koma pa nthawiyi nʼkuti mkaziyo atatenga amuna awiriwo ndi kuwabisa. Tsono anayankha kuti, “Inde, anthuwo anafikadi ku nyumba kuno. Koma sindinadziwe kumene anachokera.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:4
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? Ngati mzinda ndi uwu? Munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya.


Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino.


Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina?


Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.


ndipo m'mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.


Koma mzindawo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.


Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa