Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 2:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo m'mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo m'mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Kuno achoka ndi chisisira, chipata cha mzinda uno chili pafupi kutsekedwa. Sindidaŵafunse kumene akupita, koma mukaŵalondola, mungathe kuŵapeza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iwo achoka kuno ndi chisisira, chipata cha mzinda chili pafupi kutsekedwa. Ndiye sindidziwa kumene alowera. Koma mukawalondola msanga muwapeza.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:5
11 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata.


Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.


Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.


Ndipo kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya, osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ake atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa.


Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwe uko afuma;


Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi.


Ndipo amunawo anawalondola panjira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata.


Ndipo pazipata zake sipatsekedwa konse usana, (pakuti sikudzakhala usiku komweko);


Ndipo pamene Saulo anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, Iye alikudwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa