Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 2:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pomwepo mfumuyo idatuma anthu kwa Rahabu kukamuuza kuti, “Anthu amene ali m'nyumba mwakowo abwera kudzazonda dziko lonseli, tsono atulutse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho Mfumu ya Yeriko inatumiza uthenga kwa Rahabe kuti, “Atulutse anthu amene abwera ku nyumba kwakowo chifukwa iwo abwera kuti adzazonde dzikoli.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 2:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.


Koma ife tinati kwa iye, Tili anthu oona; sitili ozonda;


Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula?


Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.


akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?


Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka? Natulutsidwa tsiku la mkwiyo?


Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe.


Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.


Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.


Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende.


Ndipo anatero, natulutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni.


Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israele, kulizonda dziko.


Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwe uko afuma;


Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa