Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:26 - Buku Lopatulika

26 Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Ndili ndi zambiri zoti ndinene za inu, ndiponso zoti ndikutsutsireni. Koma amene adandituma ngwoona, ndipo ndimauza anthu a pansi pano zimene Iyeyo adandiwuza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:26
17 Mawu Ofanana  

Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.


Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.


chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine.


Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.


Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.


Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.


Pamenepo Yesu anafuula mu Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.


Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.


Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate.


Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite.


Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhale eya ndi iai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa