Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:18 - Buku Lopatulika

18 Ine ndine wakuchita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine achita umboni wa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ine ndine wakuchita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine achita umboni wa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ine ndimadzichitira ndekha umboni, nawonso Atate amene adandituma amandichitira umboni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:18
16 Mawu Ofanana  

Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.


Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.


Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine,


Ine ndi Atate ndife amodzi.


Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.


Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi.


Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.


Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa