Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 7:41 - Buku Lopatulika

41 Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka m'Galileya?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Ena ankanena kuti, “Ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Koma ena ankanena kuti, “Kodi Mpulumutsiyo nkuchokera ku Galileya ngati?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Ena anati, “Iye ndiye Khristu.” Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya?

Onani mutuwo Koperani




Yohane 7:41
11 Mawu Ofanana  

Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).


Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.


Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.


Koma ameneyo tidziwa uko achokera: koma Khristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera.


Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?


Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa