Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:61 - Buku Lopatulika

61 Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

61 Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

61 Yesu adaadziŵa mumtima mwake kuti ophunzira ake akung'ung'udza za zimenezi. Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi zimenezi mukukhumudwa nazo?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

61 Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani?

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:61
8 Mawu Ofanana  

Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.


Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?


Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.


Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.


Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.


Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa