Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 6:30 - Buku Lopatulika

30 Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Iwo adafunsanso kuti, “Mungatiwonetse chizindikiro chotani kuti tikachiwona tikukhulupirireni? Nanga muchitapo chiyani?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani?

Onani mutuwo Koperani




Yohane 6:30
22 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.


Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la paguwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova.


Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi.


Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka.


amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe!


Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.


Ndipo Afarisi anatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye.


Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate.


Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirire Iye;


Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?


Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya.


Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.


Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.


Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.


m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru:


pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa