Yohane 21:23 - Buku Lopatulika23 Chifukwa chake mau awa anatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Chifukwa chake mau awa anatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Tsono mbiri idamveka pakati pa abale kuti wophunzira mnzaoyo sadzafa. Komatu Yesu sadamuuze kuti sadzafa ai, koma adaati, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?” Onani mutuwo |