Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 19:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Akulu a ansembe ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja ataona Yesu, adafuula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Pilato adaŵauza kuti, “Mtengeni inuyo mukampachike, ine ndiye sindikumpeza chifukwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:6
15 Mawu Ofanana  

Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro.


Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.


Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha.


Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.


Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.


Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge Iye inu, ndi kumweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda anati kwa iye, Tilibe ulamuliro wakupha munthu aliyense;


Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye.


Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.


Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse.


ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa