Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 19:23 - Buku Lopatulika

23 Pamenepo asilikali, m'mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Pamenepo asilikali, m'mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Asilikali aja atapachika Yesu, adatenga zovala zake, nazigaŵa panai, msilikali aliyense chigawo chake. Adatenganso mkanjo wake. Mkanjowo unali wolukidwa kuyambira pamwamba mpaka pansi, opanda msoko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:23
6 Mawu Ofanana  

Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.


Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere:


Ndipo anampachika Iye, nagawana zovala zake mwa iwo okha, ndi kuchita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani.


Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.


Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa