Yohane 19:24 - Buku Lopatulika24 Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Tsono asilikaliwo adauzana kuti, “Tisaung'ambe, koma tichite mayere kuti tiwone ukhala wa yani.” Zidaayenda choncho kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Adagaŵana zovala zanga, ndipo mkanjo wanga adauchitira mayere.” Zimenezi adachitadi asilikali aja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge.” Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati, “Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo ndi kuchita maere pa zovala zangazo.” Choncho izi ndi zimene asilikali anachita. Onani mutuwo |