Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 16:7 - Buku Lopatulika

7 Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Komabe ndikukuuzani zoona, kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti ndichoke. Pakuti ngati sindichoka, Nkhoswe ija siidzabwera kwa inu. Koma ngati ndipita, ndidzaitumiza kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 16:7
19 Mawu Ofanana  

Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.


Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.


Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;


Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.


Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.


Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine.


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.


Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro;


Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho;


Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa