Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 15:22 - Buku Lopatulika

22 Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ndikadapanda kubwera ndi kulankhula nawo, sakadakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nkukanira mlandu wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 15:22
17 Mawu Ofanana  

Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.


mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira.


Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.


Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.


Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.


za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine;


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.


Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima;


Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;


Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.


Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.


monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa