Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 13:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Yudasi atangolandira mkatewo, Satana adaloŵa mwa iye. Yesu adamuuza kuti, “Zimene ufuna kuchita, kachite mwamsanga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye. Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 13:27
16 Mawu Ofanana  

Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.


Muike munthu woipa akhale mkulu wake; ndi mdani aime padzanja lamanja lake.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi.


Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale.


Ndipo Satana analowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo.


Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,


Koma palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa chimene anafuna, poti atere naye.


Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?


Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa