Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 11:44 - Buku Lopatulika

44 Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adaŵauza kuti, “Mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu. Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:44
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.


Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.


Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu;


Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.


Ine ndi Atate ndife amodzi.


Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.


Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau aakulu, Lazaro, tuluka.


Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.


ndipo m'mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowemo.


ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.


Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.


ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.


Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa