Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 11:39 - Buku Lopatulika

39 Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Tsono adati, “Tachotsani chimwalacho.” Marita, mlongo wa womwalirayo, adamuuza kuti, “Pepani Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wagonamo masiku anai.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Yesu anati, “Chotsani mwala.” Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:39
11 Mawu Ofanana  

Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa.


kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.


Kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi.


Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda?


Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai.


Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;


Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,


koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?


amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa